GANIZO LENILENI MWA CHIDULE (Chichewa Abstract; translated by Dalitso Richard Kafumbata)
Kufikira lero, pali mitundu ya nsomba za m'gulu la mbuna, chisawasawa,
ndunduma, utaka, ncheni, gundamwala, kabibi ndi zina zotero yokwana
pafupifupi mazana atatu ndi mphambu makumi atatu yomwe ili yodziwika
bwinobwino. Nsomba zimenezi zimapezeka mu nyanja ya Malawi yokha muno
mu Africa ndi pa dziko lonse lapansi. Komabe pali mitundu ya nsomba zomwezi
yochuluka kwambiri yomwe sinadziwike kwenikweni. Pano ndikufuna
kufotokoza za nsomba ina ya tsopano ya m'gulu lomweli yomwe imapezeka
m'malo akuya mu nyanja ya Malawi. Nsombayi ndaiphatika mu mtundu
wotchedwa Otopharynx. Nsombayi ili ndi madontho atatu mnthiti mwake ndi
mano okhuthala okhala ndii nsonga ziwiri. Nsombayi ndi yokulupala ndipo
ikusiyana ndi nsomba zina za madontho atatu zopezekanso m'gululi chifukwa cha
mlomo wake womwe ndi wochindikala wangowe. Mlomo woterewu
ungagwiritsidwe ntchito ngati lilime pomvera kakomedwe ndi kawawidwe ka
chakudya. Ndifotokozanso za khalidwe ndi maonekedwe ena a nsombayi omwe
akuyisiyanitsa ndi nsomba zinzake za m'gululi. Makhazikitsidwe a khalidwe ndi
maonekedwe a nsomba za m'gulu la Otopharynx amasiyana ndi nsomba zina
zonse za m'gulu la mbuna, chisawasawa, ndunduma, utaka, ncheni, gundamwala,
kabibi ndi zina zotero. Pa chifukwa ichi gulu limeneli likuoneka ngati ndiloima
palokha. Ngakhale izi zili chonchi, gulu limeneli ndilovomerezeka pakali pano
ndipo likuthandiza pa chintchito choika nsomba zooneka zofananafanana
m'makhalidwe ndi m'maonekedwe m'magulu osiyana.